Ndipo sanamzindikire iye, chifukwa kuti manja ake anali aubweya, onga manja a Esau mkulu wake; ndipo anamdalitsa iye.
Genesis 27:24 - Buku Lopatulika Ndipo anati, Kodi ndiwe mwana wanga weniweni Esau? Ndipo anati, Ndine amene. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati, Kodi ndiwe mwana wanga weniweni Esau? Ndipo anati, Ndine amene. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma adafunsanso kuti, “Kodi ndiwedi mwana wanga Esau?” Yakobe adayankhanso kuti, “Ndine amene.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Isake anafunsa, “Kodi ndiwedi mwana wanga Esau?” Yakobo anayankha, “Inde ndine.” |
Ndipo sanamzindikire iye, chifukwa kuti manja ake anali aubweya, onga manja a Esau mkulu wake; ndipo anamdalitsa iye.
Ndipo iye anati, Usendere nayo kwa ine, ndidye nyama ya mwana wanga, kuti moyo wanga ukudalitse iwe. Ndipo anasendera nayo kwa iye, nadya iye; ndipo anamtengera vinyo, namwa iye.
Ndipo mfumuyo inanena naye, Usowanji? Iye nayankha, Zoonadi ine ndine mkazi wamasiye, mwamuna wanga anamwalira.
Ndipo anati kwa iye, Inenso ndine mneneri wonga iwe, ndipo mthenga analankhula ndi ine mwa mau a Yehova, nati, Kambwezere kwanu, kuti akadye mkate, namwe madzi. Koma anamnamiza.
Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera;
Izi ndizo muzichite: Nenani choonadi yense ndi mnzake; weruzani zoona ndi chiweruzo cha mtendere m'zipata zanu;
Mwa ichi, mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzake; pakuti tili ziwalo wina ndi mnzake.
musamanamizana wina ndi mnzake; popeza mudavula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake,
Nasanduliza makhalidwe ake pamaso pao, nadzionetsera m'manja mwao ngati wamisala, nangolembalemba pa zitseko za chipata, nakhetsa dovu lake pa ndevu yake.
Nati Davide kwa Ahimeleki wansembeyo, Mfumu inandilamulira ntchito, ninena nane, Asadziwe munthu aliyense kanthu za ntchito imene ndakutumira ndi kukulamulira; ndipo ndawapanga anyamatawo ku malo akuti.
Ndipo Akisi anati, Waponyana nkhondo ndi yani lero? Nati Davide, Ndi a kumwera kwa Ayuda, ndi a kumwera kwa Ayerameele, ndi a kumwera kwa Akeni.