Kapena atate wanga adzandiyambasa, ndipo ndidzaoneka pamaso pake ngati wakunyenga; pamenepo ndidzadzitengera ine temberero, si mdalitso.
Genesis 27:22 - Buku Lopatulika Ndipo Yakobo anasendera kwa Isaki atate wake, ndipo anamyambasa nati, Mau ndi mau a Yakobo, koma manja ndi manja a Esau. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yakobo anasendera kwa Isaki atate wake, ndipo anamyambasa nati, Mau ndi mau a Yakobo, koma manja ndi manja a Esau. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yakobe adasendera pafupi ndi bambo wake, ndipo bambo wakeyo adamukhudza nati, “Liwuli ndi la Yakobe, koma mikonoyi ndi ya Esau.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yakobo anasendera kufupi ndi abambo ake Isake ndipo anamukhudza nati, “Mawuwa ndi mawu a Yakobo koma mikonoyi ndi mikono ya Esau.” |
Kapena atate wanga adzandiyambasa, ndipo ndidzaoneka pamaso pake ngati wakunyenga; pamenepo ndidzadzitengera ine temberero, si mdalitso.
Ndipo Isaki anati kwa Yakobo, Sendera kuno, ndikuyambase mwana wanga, ngati ndiwe mwana wanga Esau ndithu, kapena wina.
Ndipo sanamzindikire iye, chifukwa kuti manja ake anali aubweya, onga manja a Esau mkulu wake; ndipo anamdalitsa iye.
Pokhala iwo m'nyumba ya Mika, anazindikira mau a mnyamata Mleviyo, napatukirako, nanena naye, Anadza nawe kuno ndani? Uchitanji muno? Ukhala nacho chiyani kuno?