Kapena atate wanga adzandiyambasa, ndipo ndidzaoneka pamaso pake ngati wakunyenga; pamenepo ndidzadzitengera ine temberero, si mdalitso.
Genesis 27:21 - Buku Lopatulika Ndipo Isaki anati kwa Yakobo, Sendera kuno, ndikuyambase mwana wanga, ngati ndiwe mwana wanga Esau ndithu, kapena wina. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Isaki anati kwa Yakobo, Sendera kuno, ndikuyambase mwana wanga, ngati ndiwe mwana wanga Esau ndithu, kapena wina. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Isaki adauza Yakobe kuti, “Tasendera pafupi kuti ndikukhudze, kuti ndidziŵe ngati ndiwedi mwana wanga Esau, kapena ai.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Isake anati kwa Yakobo, “Tabwera pafupi ndikukhudze mwana wanga, kuti ndidziwedi ngati uli mwana wanga Esau kapena ayi.” |
Kapena atate wanga adzandiyambasa, ndipo ndidzaoneka pamaso pake ngati wakunyenga; pamenepo ndidzadzitengera ine temberero, si mdalitso.
Ndipo Yakobo anasendera kwa Isaki atate wake, ndipo anamyambasa nati, Mau ndi mau a Yakobo, koma manja ndi manja a Esau.
Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu. Ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine, kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.
Ndilenga chipatso cha milomo, Mtendere, mtendere kwa iye amene ali kutali, ndi kwa iye amene ali chifupi, ati Yehova; ndipo ndidzamchiritsa iye.
Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.