Ndipo anamuka nakatenga nadza nato kwa amake; amake ndipo anakonza chakudya chokolera chonga chimene anachikonda atate wake.
Genesis 27:17 - Buku Lopatulika ndipo anapereka m'dzanja la mwana wake Yakobo chakudya chokoleracho, ndi mikate imene anaipanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo anapereka m'dzanja la mwana wake Yakobo chakudya chokoleracho, ndi mikate imene anaipanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo adatenga buledi ndi chakudya chokonza bwino chija, napatsira Yakobe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka, anamupatsa Yakobo chakudya chokoma chija chimene anaphika pamodzi ndi buledi. |
Ndipo anamuka nakatenga nadza nato kwa amake; amake ndipo anakonza chakudya chokolera chonga chimene anachikonda atate wake.
Ndipo iye analowa kwa atate wake, nati, Atate wanga; iye anati, Ndine pano; ndani iwe mwana wanga?
nundikonzere ine chakudya chokolera chonga chomwe ndichikonda ine, nudze nacho kwa ine kuti ndidzadye; kuti moyo wanga ukadalitse iwe ndisanafe.