Ndipo anamuka nakatenga nadza nato kwa amake; amake ndipo anakonza chakudya chokolera chonga chimene anachikonda atate wake.
Genesis 27:15 - Buku Lopatulika Ndipo Rebeka anatenga zovala zokoma za Esau mwana wake wamkulu zinali m'nyumba, naveka nazo Yakobo mwana wake wamng'ono; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Rebeka anatenga zovala zokoma za Esau mwana wake wamkulu zinali m'nyumba, naveka nazo Yakobo mwana wake wamng'ono; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Rebeka adatenga zovala zabwino za Esau zimene ankazisunga m'nyumba, naveka mng'ono wake Yakobe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Rebeka anatenga zovala zabwino kwambiri za Esau mwana wake wamkulu zimene zinali mʼnyumba namuveka Yakobo. |
Ndipo anamuka nakatenga nadza nato kwa amake; amake ndipo anakonza chakudya chokolera chonga chimene anachikonda atate wake.
Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zovala zake, namdalitsa, nati, Taona, kununkhira kwa mwana wanga, kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova;
Koma atateyo ananena kwa akapolo ake, Tulutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumveke; ndipo mpatseni mphete kudzanja lake ndi nsapato kumapazi ake;
Chenjerani nao alembi, amene afuna kuyendayenda ovala miinjiro, nakonda kupatsidwa moni m'misika, ndi mipando yaulemu m'sunagoge, ndi malo aulemu pamaphwando;