Ndipo woyamba anabadwa wofiira, mwake monse monga malaya aubweya; ndipo anamutcha dzina lake Esau.
Genesis 27:11 - Buku Lopatulika Yakobo ndipo anati kwa Rebeka amake, Taonani, Esau mkulu wanga ndiye munthu waubweya, ine ndine munthu wosalala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yakobo ndipo anati kwa Rebeka amake, Taonani, Esau mkulu wanga ndiye munthu waubweya, ine ndine munthu wosalala. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Yakobe adauza mai wake kuti, “Mukudziŵa kuti Esau ndi wacheya, koma ine khungu langa ndi losalala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Yakobo anati kwa Rebeka amayi ake, “Komatu mʼbale wanga Esau ndi munthu wa khungu la ubweya zedi, ndipo ine ndine munthu wa khungu losalala. |
Ndipo woyamba anabadwa wofiira, mwake monse monga malaya aubweya; ndipo anamutcha dzina lake Esau.
Ndipo sanamzindikire iye, chifukwa kuti manja ake anali aubweya, onga manja a Esau mkulu wake; ndipo anamdalitsa iye.