Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi thumba la madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.
Genesis 26:33 - Buku Lopatulika Ndipo anatcha dzina lake Siba, chifukwa chake dzina la mzindawo ndi Beereseba kufikira lero lino. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anatcha dzina lake Siba, chifukwa chake dzina la mudziwo ndi Beereseba kufikira lero lino. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Isaki adachitcha Siba. Nchifukwa chake mzindawo umatchedwa Beereseba mpaka lero lino. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye chitsimecho anachitcha Pangano. Nʼchifukwa chake mzindawu umatchedwa Beeriseba mpaka lero. |
Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi thumba la madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.
Ndipo iwo anati, Kuona tinaona kuti Yehova ali ndi iwe; ndipo tinati, Tilumbiriranetu tonse awiri, ife ndi iwe, tichite pangano ndi iwe;
Ndipo panali tsiku lomwelo anyamata ake a Isaki anadza namuuza iye za chitsime chimene anakumba, nati kwa iye, Tapeza madzi.
koma musamafuna Betele, kapena kumalowa mu Giligala; musamapita ku Beereseba; pakuti Giligala adzalowadi m'ndende, ndi Betele adzasanduka chabe.