Ndipo anawaumiriza iwo ndithu: ndipo anapatukira kwa iye, nalowa m'nyumba mwake; ndipo anawakonzera iwo madyerero, naphika mikate yopanda chotupitsa, ndipo anadya.
Genesis 26:30 - Buku Lopatulika Ndipo anakonzera iwo madyerero, ndipo anadya namwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anakonzera iwo madyerero, ndipo anadya namwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Isaki adaŵakonzera phwando, ndipo anthuwo adadya ndi kumwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Isake anawakonzera phwando, ndipo anadya ndi kumwa. |
Ndipo anawaumiriza iwo ndithu: ndipo anapatukira kwa iye, nalowa m'nyumba mwake; ndipo anawakonzera iwo madyerero, naphika mikate yopanda chotupitsa, ndipo anadya.
Ndipo anakula mwanayo naletsedwa kuyamwa: ndipo Abrahamu anakonza madyerero aakulu tsiku lomwe analetsedwa Isaki kuyamwa.
Ndipo analawira m'mamawa nalumbirirana wina ndi mnzake; ndipo Isaki anawalola amuke, ndipo anauka kuchokera kwa iye m'mtendere.
Ndipo Yakobo anapereka nsembe paphiripo, naitana abale ake kuti adye chakudya; ndipo anadya chakudya, nagona paphiripo usiku wonse.
Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anamtengera Mulungu nsembe yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo Aroni ndi akulu onse a Israele anadza kudzadya mkate ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu.
Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye: