ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;
Genesis 26:29 - Buku Lopatulika kuti usatichitire ife zoipa, pakuti sitidakhudze iwe, sitidakuchitire kanthu koma kabwino ndiko, ndipo takulola umuke ndi mtendere; ndiwe tsopano wodalitsidwa ndi Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti usatichitire ife zoipa, pakuti sitidakhudza iwe, sitidakuchitira kanthu koma kabwino ndiko, ndipo takulola umuke ndi mtendere; ndiwe tsopano wodalitsidwa ndi Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa kuti simudzatichita zoipa, monga ife sitidakuchiteni zoipa. Tidakuchitirani zabwino, ndipo tidakulolani kuti mupite mwamtendere. Tsopano Chauta wakudalitsani.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kuti inu simudzatichitira zoyipa monga ifenso sitinakuchitireni nkhondo. Ife tinakuchitirani zabwino zokhazokha, ndipo tinakulolani kuti musamuke kuchoka kwathu mu mtendere. Tsopano Yehova wakudalitsani.” |
ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;
ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.
Ndipo panali nthawi yomweyo, Abimeleki ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yake anati kwa Abrahamu, kuti, Mulungu ali pamodzi ndi iwe m'zonse uzichita iwe;
kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja; ndipo mbeu zako zidzagonjetsa chipata cha adani ao;
Ndipo anati, Talowa iwe, wodalitsidwa ndi Yehova; uimiriranji kunjako? Chifukwa kuti ndakonzeratu nyumba, ndi malo a ngamira.