ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.
Genesis 26:28 - Buku Lopatulika Ndipo iwo anati, Kuona tinaona kuti Yehova ali ndi iwe; ndipo tinati, Tilumbiriranetu tonse awiri, ife ndi iwe, tichite pangano ndi iwe; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwo anati, Kuona tinaona kuti Yehova ali ndi iwe; ndipo tinati, Tilumbiriranetu tonse awiri, ife ndi iwe, tichite pangano ndi iwe; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwowo adayankha kuti, “Tsopano tikudziŵa kuti Chauta ali nanu, ndipo taganiza zoti inu ndi ife tichite chipangano. Tikufuna kuti inu mulonjeze Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anayankha, “Tsopano tadziwa kuti Yehova anali ndi iwe; ndiye taganiza kuti inu ndi ife tichite lumbiro. Ife tichite pangano ndi inu |
ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.
ukatero udzakhala wosachimwa pa malumbiro ako, pofika iwe kwa abale anga; ndipo ngati sadzakupatsa iwe, udzakhala wosachimwa pa malumbiro ako.
Ndipo mbuyake anaona kuti Yehova anali ndi iye, ndi kuti Yehova anamlemereza m'dzanja lake zonse anazichita.
Ndipo panali chiyambire anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yake, ndi pa zake zonse, Yehova anadalitsa nyumba ya Mwejipito chifukwa cha Yosefe; ndipo mdalitso wa Yehova unali pa zake zonse, m'nyumba ndi m'munda.
Ndipo Solomoni mwana wa Davide analimbikitsidwa mu ufumu wake, ndipo Yehova Mulungu wake anali naye, namkuza kwakukulu.
Namemeza onse a mu Yuda ndi mu Benjamini, ndi iwo akukhala nao ochokera ku Efuremu, ndi Manase, ndi Simeoni; pakuti anamdzera ochuluka ochokera ku Israele, pamene anaona kuti Yehova Mulungu wake anali naye.
Atero Yehova, Ntchito ya Ejipito, ndi malonda a Kusi, ndi a Seba, amuna amsinkhu adzakugonjera, nadzakhala ako; nadzakutsata pambuyo m'maunyolo; adzakugonjera, nadzakugwira; adzakupembedza ndi kunena, Zoona Mulungu ali mwa iwe; ndipo palibenso wina, palibe Mulungu.
Ndipo ana aamuna a iwo amene anavuta iwe adzafika, nadzakugwadira; ndipo iwo onse amene anakuchepetsa iwe adzagwadira kumapazi ako, nadzakutcha iwe, Mzinda wa Yehova, Ziyoni wa Woyera wa Israele.
Koma inu mudzatchedwa ansembe a Yehova; anthu adzakuyesani inu atumiki a Mulungu wathu; inu mudzadya chuma cha amitundu, nimudzalowa mu ulemerero wao.
Ndipo ana ao adzadziwidwa mwa amitundu, ndi obadwa ao mwa anthu; onse amene awaona adzawazindikira kuti iwo ndiwo ana amene Yehova wadalitsa.
zobisika za mtima wake zionetsedwa; ndipo chotero adzagwa nkhope yake pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu.
Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.
Pakuti anthu amalumbira pa wamkulu; ndipo m'chitsutsano chao chilichonse lumbiro litsiriza kutsimikiza.
Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndidzayamba kukukuza pamaso pa Aisraele onse, kuti adziwe, kuti monga momwe ndinakhalira ndi Mose, momwemo ndidzakhala ndi iwe.
Pamenepo Nahasi Mwamoni anakwera, namanga Yabesi-Giliyadi zithando; ndipo anthu onse a ku Yabesi anati kwa Nahasi, Mupangane chipangano ndi ife, ndipo tidzakutumikirani inu.
Ndipo Saulo anaona, nadziwa kuti Yehova ali ndi Davide; ndi kuti Mikala mwana wa Saulo anamkonda Davide.