Ndipo ndikubalitsa iwe ndithu, ndipo ndidzakuyesa iwe mitundu, ndipo mafumu adzatuluka mwa iwe.
Genesis 26:22 - Buku Lopatulika Ndipo anachoka kumeneko nakumba chitsime china; koma sanakangane nacho chimenecho; ndipo anatcha dzina lake Rehoboti; ndipo anati, Chifukwa kuti tsopano Yehova anatipatsa ife malo, ndipo tidzabalana m'dziko muno. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anachoka kumeneko nakumba chitsime china; koma sanakangane nacho chimenecho; ndipo anatcha dzina lake Rehoboti; ndipo anati, Chifukwa kuti tsopano Yehova anatipatsa ife malo, ndipo tidzabalana m'dziko muno. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adachoka kumeneko, nakakumba chitsime china. Pa chimenechi panalibe mkangano, motero adachitcha Ufulu. Adati, “Tsopano Chauta watipatsa ufulu m'dziko, ndipo tidzalemera kuno.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anachokapo pamenepo nakakumba china. Koma apa sanakanganiranenso ndi munthu. Iye anachitcha Kutakasuka, nati, “Tsopano Yehova watipatsa ife malo otakasukirako ndipo tilemera muno.” |
Ndipo ndikubalitsa iwe ndithu, ndipo ndidzakuyesa iwe mitundu, ndipo mafumu adzatuluka mwa iwe.
Mulungu Wamphamvuyonse akudalitse iwe, akubalitse iwe, akuchulukitse iwe, kuti ukhale khamu la anthu:
Ndipo dzina la wachiwiri anamutcha Efuremu: chifukwa Mulungu anandibalitsa ine m'dziko la kusauka kwanga.
Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.
Ana a Israele ndipo anaswana, nabalana, nachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu; ndipo dziko linadzala nao.
Kuza malo a hema wako, afunyulule zinsalu za mokhalamo iwe; usaleke, tanimphitsa zingwe zako, limbitsa zikhomo zako.
Pakuti iwe udzafalikira ponse padzanja lamanja ndi lamanzere, ndipo mbeu yako idzalandira amitundu cholowa chao, ndi kukhalitsa anthu m'mabwinja.