Ndipo Abrahamu anamdzudzula Abimeleki chifukwa cha chitsime cha madzi, anyamata ake a Abimeleki anachilanda.
Genesis 26:21 - Buku Lopatulika Ndipo anakumbanso chitsime china, ndipo anakangana nachonso; natcha dzina lake Sitina. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anakumbanso chitsime china, ndipo anakangana nachonso; natcha dzina lake Sitina. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Antchito a Isaki aja adakumba chitsime china, ndipo padaukanso mkangano wina pa za chitsime chimenecho. Motero adachitcha Chidani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka iwo anakumba chitsime china, koma anakangananso chifukwa cha chitsimecho. Choncho anachitcha dzina lakuti Chidani. |
Ndipo Abrahamu anamdzudzula Abimeleki chifukwa cha chitsime cha madzi, anyamata ake a Abimeleki anachilanda.
Ndipo abusa a Gerari anakangana ndi abusa a Isaki kuti, Madzi ndi athu; ndipo anatcha dzina la chitsimecho Eseke: chifukwa anakangana naye.
Ndipo anachoka kumeneko nakumba chitsime china; koma sanakangane nacho chimenecho; ndipo anatcha dzina lake Rehoboti; ndipo anati, Chifukwa kuti tsopano Yehova anatipatsa ife malo, ndipo tidzabalana m'dziko muno.
Ndipo pokhala mfumu Ahasuwero, poyambira ufumu wake, analembera chowaneneza okhala mu Yuda ndi mu Yerusalemu.