Ndipo panali ndeu, abusa a Abramu kudana ndi abusa a Loti. Akanani ndi Aperizi ndipo analinkukhala nthawi yomweyo m'dzikomo.
Genesis 26:20 - Buku Lopatulika Ndipo abusa a Gerari anakangana ndi abusa a Isaki kuti, Madzi ndi athu; ndipo anatcha dzina la chitsimecho Eseke: chifukwa anakangana naye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo abusa a Gerari anakangana ndi abusa a Isaki kuti, Madzi ndi athu; ndipo anatcha dzina la chitsimecho Eseke: chifukwa anakangana naye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma abusa a ku Gerari adayamba kukangana ndi abusa a Isaki, ankati, “Madziŵa ndi athu.” Motero chitsimecho Isaki adachitcha Mkangano, chifukwa adakangana naye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma abusa a ku Gerari anakangana ndi abusa a Isake nati, “Madziwa ndi athu.” Motero iye anachitcha chitsimecho Mkangano chifukwa anakangana naye. |
Ndipo panali ndeu, abusa a Abramu kudana ndi abusa a Loti. Akanani ndi Aperizi ndipo analinkukhala nthawi yomweyo m'dzikomo.
Ndipo Abrahamu anamdzudzula Abimeleki chifukwa cha chitsime cha madzi, anyamata ake a Abimeleki anachilanda.
Ndipo anyamata a Isaki anakumba m'chigwa, napeza kumeneko chitsime cha madzi otumphuka.
Mudzati, Akapolo anu akhala oweta ng'ombe chiyambire ubwana wathu kufikira tsopano, ife ndi atate athu; kuti mukhale m'dziko la Goseni; chifukwa abusa onse anyansira Aejipito.