Ndipo Abrahamu anamdzudzula Abimeleki chifukwa cha chitsime cha madzi, anyamata ake a Abimeleki anachilanda.
Genesis 26:15 - Buku Lopatulika Ndipo zitsime zonse anakumba anyamata a atate wake, Abrahamuyo akali moyo, Afilisti anazitseka, nazikwirira ndi dothi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo zitsime zonse anakumba anyamata a atate wake, Abrahamuyo akali moyo, Afilisti anazitseka, nazikwirira ndi dothi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa (Anthuwo anali atakwirira zitsime zonse zimene antchito a bambo wake Abrahamu adaakumba, Abrahamuyo adakali ndi moyo.) Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi iyi nʼkuti Afilisti atakwirira ndi dothi zitsime zonse zimene antchito abambo ake Abrahamu anakumba mu nthawi ya abambo akewo. |
Ndipo Abrahamu anamdzudzula Abimeleki chifukwa cha chitsime cha madzi, anyamata ake a Abimeleki anachilanda.
Ndipo anati, Anaankhosa aakazi asanu ndi awiriwa uwalandire padzanja langa, kuti akhale mboni zanga, kuti ndakumba ine chitsime chimenechi.