Ndipo anamuka Abramu monga Yehova ananena kwa iye, ndipo Loti anamuka pamodzi naye: ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi awiri kudza zisanu, pamene anatuluka mu Harani.
Genesis 25:7 - Buku Lopatulika Masiku a zaka za moyo wake wa Abrahamu amene anakhala ndi moyo ndiwo zaka zana limodzi, kudza makumi asanu ndi limodzi, kudza khumi ndi zisanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Masiku a zaka za moyo wake wa Abrahamu amene anakhala ndi moyo ndiwo zaka zana limodzi, kudza makumi asanu ndi limodzi, kudza khumi ndi zisanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abrahamu adakhala ndi moyo zaka 175. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abrahamu anakhala ndi moyo zaka 175. |
Ndipo anamuka Abramu monga Yehova ananena kwa iye, ndipo Loti anamuka pamodzi naye: ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi awiri kudza zisanu, pamene anatuluka mu Harani.
Ndipo Isaki anatsirizika nafa, nasonkhanitsidwa kwa anthu a mtundu wake, wokalamba ndi wa masiku okwanira: ndipo Esau ndi Yakobo ana ake aamuna anamuika iye.
Ndipo Yakobo anakhala m'dziko la Ejipito zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri; ndipo masiku a Yakobo zaka za moyo wake zinali zaka zana limodzi mphambu makumi anai kudza zisanu ndi ziwiri.
Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo anga m'masiku a ulendo wao.
Ndipo anafa Yosefe, anali wa zaka zana limodzi ndi khumi; ndipo anakonza thupi lake ndi mankhwala osungira, ndipo anamuika iye m'bokosi mu Ejipito.