Genesis 25:2 - Buku Lopatulika Ndipo anambalira iye Zimirani ndi Yokisani ndi Medani, ndi Midiyani, ndi Isibaki, ndi Suwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anambalira iye Zimirani ndi Yokisani ndi Medani, ndi Midiyani, ndi Isibaki, ndi Suwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ketura adamubalira Zimirani, Yokisani, Medani, Midiyani, Isibaki ndi Suwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iyeyu anamubalira Zimurani, Yokisani, Medani, Midiyani, Isibaki ndi Suwa. |
Ndipo Yokisani anabala Sheba, ndi Dedani. Ana a Dedani ndi Aasuri, ndi Aletusi, ndi Aleumi.
Ndipo Husamu anamwalira, ndipo Hadadi mwana wamwamuna wa Bedadi, amene anakantha Midiyani m'dambo la Mowabu, analamulira m'malo mwake: dzina la mzinda wake ndi Aviti.
Ndipo anapita pamenepo Amidiyani a malonda: ndipo anamtulutsa namkweza Yosefe m'dzenjemo, namgulitsa kwa Aismaele ndi masekeli a siliva makumi awiri; ndipo ananka naye Yosefe ku Ejipito.
Amidiyani ndipo anamgulitsa iye anke ku Ejipito kwa Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda.
Ndipo anachoka ku Midiyani nafika ku Parani, natenga anthu a ku Parani pamodzi nao, nafika ku Ejipito kwa Farao mfumu ya Aejipito, ameneyo anampatsa nyumba, namnenera zakudya, nampatsako dziko.
Atamva tsono mabwenzi atatu a Yobu za choipa ichi chonse chidamgwera, anadza, yense kuchokera kwao, Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, napangana kudzafika kumlirira ndi kumsangalatsa.
Ndipo Mowabu anati kwa akulu a Midiyani, Tsopano msonkhano uwu udzanyambita zonse zili pozinga pathu, monga ng'ombe zinyambita msipu wa kubusa. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anali mfumu ya Mowabu masiku amenewo.
Abwezereni chilango Amidiyani chifukwa cha ana a Israele; utatero udzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wako.
Ndipo anapha mafumu a Amidiyani pamodzi ndi ophedwa ao ena; ndiwo Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri, ndi Reba, mafumu asanu a Amidiyani; namupha Balamu mwana wa Beori ndi lupanga.