Koma za Ismaele, ndamvera iwe: taona, ndamdalitsa iye, ndipo ndidzamchulukitsa iye ndithu; adzabala akalonga khumi ndi awiri, ndipo ndidzamuyesa iye mtundu waukulu.
Genesis 25:16 - Buku Lopatulika ana a Ismaele ndi awa: maina ao m'midzi yao, m'misasa yao ndi awa: akalonga khumi ndi awiri m'mitundu yao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ana a Ismaele ndi awa: maina ao m'midzi yao, m'misasa yao ndi awa: akalonga khumi ndi awiri m'mitundu yao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ameneŵa ndiwo ana a Ismaele malinga ndi midzi yao ndiponso zigono zao. Anali mafumu khumi ndi aŵiri a mafuko osiyana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amenewa ndi ana a Ismaeli ndi mayina awo monga mwa midzi ndi misasa yawo. Anali olamulira mafuko khumi ndi awiri. |
Koma za Ismaele, ndamvera iwe: taona, ndamdalitsa iye, ndipo ndidzamchulukitsa iye ndithu; adzabala akalonga khumi ndi awiri, ndipo ndidzamuyesa iye mtundu waukulu.
Ndipo Abrahamu anatenga Ismaele mwana wake ndi onse amene anabadwa m'nyumba mwake, ndi onse amene anagulidwa ndi ndalama zake, amuna onse a mwa anthu a kunyumba kwake kwa Abrahamu, nadula khungu lao tsiku lomwelo, monga Mulungu ananena naye.
Pokhala pao tsono monga mwa madera ao m'malire mwao ndi awa: kwa ana a Aroni a mabanja a Akohati, pakuti maere oyamba adagwera iwowa,