Koma za Ismaele, ndamvera iwe: taona, ndamdalitsa iye, ndipo ndidzamchulukitsa iye ndithu; adzabala akalonga khumi ndi awiri, ndipo ndidzamuyesa iye mtundu waukulu.
Genesis 25:12 - Buku Lopatulika Mibadwo ya Ismaele mwana wamwamuna wa Abrahamu, amene Hagara Mwejipito mdzakazi wa Sara anambalira Abrahamu ndi iyi: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mibadwo ya Ismaele mwana wamwamuna wake wa Abrahamu, amene Hagara Mwejipito mdzakazi wa Sara anambalira Abrahamu ndi iyi: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nazi zidzukulu za Ismaele, mwana wa Abrahamu amene adamubalira Hagara, mdzakazi wa ku Ejipito uja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nazi zidzukulu za Ismaeli, mwana wa Abrahamu amene wantchito wa Sara, Hagara Mwigupto uja, anaberekera Abrahamu. |
Koma za Ismaele, ndamvera iwe: taona, ndamdalitsa iye, ndipo ndidzamchulukitsa iye ndithu; adzabala akalonga khumi ndi awiri, ndipo ndidzamuyesa iye mtundu waukulu.
Tauka, nuukitse mnyamatayo, ndi kumgwira m'dzanja lako; chifukwa ndidzamuyesa iye mtundu waukulu.
Mibadwo yao ndi awa; woyamba wa Ismaele Nebayoti; ndi Kedara ndi Adibeele, ndi Mibisamu,
Gideoni anatinso kwa iwo, Mundilole ndipemphe kanthu kamodzi kwa inu, mundipatse aliyense maperere mwa zofunkha zanu; pakuti anali nao maperere agolide, pokhala anali Aismaele.