Genesis 25:10 - Buku Lopatulika munda umene anagula Abrahamu kwa ana a Hiti. Pamenepo anamuika Abrahamu ndi Sara mkazi wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 munda umene anagula Abrahamu kwa ana a Hiti: pamenepo anamuika Abrahamu ndi Sara mkazi wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Unali munda umene Abrahamu adaagula kwa Ahiti. Abrahamu ndi mkazi wake Sara adaikidwa kumeneko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero uwu ndi munda umene Abrahamu anagula kwa Ahiti. Kumeneko Abrahamu anakayikidwa pamodzi ndi mkazi wake Sara. |
Ndipo Abrahamu anamvera Efuroni, ndipo Abrahamu anamuyesera Efuroni ndalama zimene ananena alinkumva ana a Hiti, masekeli a siliva mazana anai, ndalama zomwezo agulana nazo malonda.
Ndipo munda wa Efuroni umene unali mu Makipela, umene unali patsogolo pa Mamure, munda ndi phanga lili momwemo, ndi mitengo yonse inali m'mundamo, yokhala m'malire monse mozungulira momwemo,
Ndipo ana a Hiti analimbitsira Abrahamu munda, ndi phanga lili m'menemo, likhale lake lamanda.
kuti andipatse ine phanga la Makipela, limene lili pansonga pamunda wake; pa mtengo wake wonse andipatse pakati pa inu, ndikhale nao manda.
koma pamene ndidzagona ndi makolo anga, udzanditenge ine kutuluka m'dziko la Ejipito, ukandiike ine m'manda mwao. Ndipo iye anati, Ndidzachita monga mwanena.
pamenepo anaika Abrahamu ndi Sara mkazi wake; pamenepo anaika Isaki ndi Rebeka mkazi wake: pamenepo ndinaika Leya: