Ndipo Isaki anamlowetsa mkaziyo m'hema wa amake Sara, namtenga Rebeka, nakhala iye mkazi wake; ndipo anamkonda iye; ndipo Isaki anatonthozedwa mtima atafa amake.
Genesis 25:1 - Buku Lopatulika Ndipo Abrahamu anatenga mkazi wina dzina lake Ketura. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abrahamu anatenga mkazi wina dzina lake Ketura. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abrahamu adakwatiranso mkazi wina dzina lake Ketura. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abrahamu anakwatira mkazi wina dzina lake Ketura. |
Ndipo Isaki anamlowetsa mkaziyo m'hema wa amake Sara, namtenga Rebeka, nakhala iye mkazi wake; ndipo anamkonda iye; ndipo Isaki anatonthozedwa mtima atafa amake.
Ndipo anambalira iye Zimirani ndi Yokisani ndi Medani, ndi Midiyani, ndi Isibaki, ndi Suwa.
Ndipo Isaki anamuitana Yakobo, namdalitsa iye, namuuza iye, nati kwa iye, Usatenge mkazi wa ana aakazi a Kanani.