Ndipo mnyamatayo anatenga ngamira khumi za mbuyake, namuka: chifukwa kuti chuma chonse cha mbuyake chinali m'dzanja lake: ndipo anachoka namuka ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori.
Genesis 24:9 - Buku Lopatulika Ndipo mnyamatayo anaika dzanja lake pansi pa ntchafu yake ya Abrahamu Mbuye wake, namlumbirira iye za chinthucho. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mnyamatayo anaika dzanja lake pansi pa ntchafu yake ya Abrahamu Mbuye wake, namlumbirira iye za chinthucho. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero wantchitoyo adaika dzanja lake m'kati mwa ntchafu za Abrahamu mbuye wake, ndipo adalumbira kuti, “Ndidzachita zonse zimene mwanenazi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho wantchitoyo anayika dzanja lake pansi pa ntchafu ya mbuye wake Abrahamu nalumbira kwa iye kuti adzachitadi monga mwa mawu a Abrahamu. |
Ndipo mnyamatayo anatenga ngamira khumi za mbuyake, namuka: chifukwa kuti chuma chonse cha mbuyake chinali m'dzanja lake: ndipo anachoka namuka ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori.
Ndipo Abrahamu anati kwa mnyamata wake wamkulu wa pa nyumba yake, amene analamulira pa zonse anali nazo, Taikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga: