Ndipo anati kwa mnyamata, Munthuyo ndani amene ayenda m'munda kukomana ndi ife? Mnyamatayo ndipo anati, Uyo ndi mbuyanga: chifukwa chake namwali anatenga chophimba chake nadziphimba.
Genesis 24:66 - Buku Lopatulika Mnyamatayo ndipo anamuuza Isaki zonse anazichita. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mnyamatayo ndipo anamuuza Isaki zonse anazichita. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Wantchitoyo adamufotokozera Isaki zonse zimene zidaachitika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono wantchito uja anawuza Isake zonse zimene anazichita. |
Ndipo anati kwa mnyamata, Munthuyo ndani amene ayenda m'munda kukomana ndi ife? Mnyamatayo ndipo anati, Uyo ndi mbuyanga: chifukwa chake namwali anatenga chophimba chake nadziphimba.
Ndipo Isaki anamlowetsa mkaziyo m'hema wa amake Sara, namtenga Rebeka, nakhala iye mkazi wake; ndipo anamkonda iye; ndipo Isaki anatonthozedwa mtima atafa amake.
Ndipo atumwi anasonkhana kwa Yesu; namuuza zilizonse adazichita, ndi zonse adaziphunzitsa.