Genesis 24:62 - Buku Lopatulika Ndipo Isaki anadzera njira ya Beere-Lahai-Roi; chifukwa kuti anakhala iye m'dziko la kumwera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Isaki anadzera njira ya Beere-Lahai-Roi; chifukwa kuti anakhala iye m'dziko la kumwera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Isaki anali atachoka kuchipululu kumene kunali chitsime cha Wamoyo-Wondipenya chija, kukakhala m'chigawo chakumwera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa nthawiyi nʼkuti Isake atafika kuchokera ku chitsime cha Wamoyo Wondipenya (Beeri-lahai-roi), popeza tsopano ankakhala ku Negevi. |
Chifukwa chake chitsimecho chinatchedwa Beere-Lahai-Roi; taonani chili pakati pa Kadesi ndi Beredi.
Abrahamu ndipo anachoka kumeneko kunka ku dziko la kumwera, ndipo anakhala pakati pa Kadesi ndi Suri, ndipo anakhala ngati mlendo mu Gerari.
Ndipo adauka Rebeka ndi anamwali ake, nakwera pa ngamira natsata munthuyo: mnyamatayo ndipo anamtenga Rebeka namuka.
Ndipo panali atafa Abrahamu, Mulungu anamdalitsa Isaki mwana wake; ndipo Isaki anakhala pa Beere-Lahai-Roi.