Ndipo anati kwa ine, Yehova, amene ndiyenda ine pamaso pake, adzatumiza mthenga wake pamodzi ndi iwe, nadzakuyendetsa bwino m'njira yako; ndipo ukamtengere mwana wanga mkazi wa mwa abale anga ndi kunyumba ya atate wanga;
Genesis 24:56 - Buku Lopatulika Ndipo iye anati kwa iwo, Musandichedwetse ine, pakuti Yehova wandiyendetsa bwino m'njira yanga: mundilole ine ndinke kwa mbuyanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye anati kwa iwo, Musandichedwetse ine, pakuti Yehova wandiyendetsa bwino m'njira yanga: mundilole ine ndinke kwa mbuyanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma wantchitoyo adati, “Chonde musandichedwetse. Chauta wandithandiza kwambiri pa ulendo wangawu. Loleni tsono ndibwerere kwa mbuyanga.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma iye anawawuza kuti, “Chonde musandichedwetse. Yehova wandithandiza kale pa ulendo wanga. Mundilole ndibwerere kwa mbuye wanga.” |
Ndipo anati kwa ine, Yehova, amene ndiyenda ine pamaso pake, adzatumiza mthenga wake pamodzi ndi iwe, nadzakuyendetsa bwino m'njira yako; ndipo ukamtengere mwana wanga mkazi wa mwa abale anga ndi kunyumba ya atate wanga;
Ndipo anadya namwa iye ndi anthu amene anali pamodzi naye, nagonapo usiku: ndipo anauka m'mamawa, ndipo iye anati, Mundilole ine ndinke kwa mbuyanga.
Ndipo panali pamene Rakele anabala Yosefe, Yakobo anati kwa Labani, Undisudzule ine ndinke kwathu ku dziko langa.
Ine, ngakhale Ine ndanena; inde ndamwitana iye, ndamfikitsa, ndipo adzapindula nayo njira yake.
Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru.