Genesis 24:52 - Buku Lopatulika Ndipo panali pamene anamva mauwo mnyamata wa Abrahamu, anamgwadira Yehova pansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali pamene anamva mauwo mnyamata wa Abrahamu, anamgwadira Yehova pansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Wantchito wa Abrahamu uja atamva mau ao aja, adaŵeramitsa mutu napembedza Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wantchito wa Abrahamu uja atamva zimene anawerama pansi pamaso pa Yehova. |
Ndipo ndinawerama mutu wanga ndi kulambira Yehova, ndi kumyamikira Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, amene ananditsogolera ine m'njira yakuona, kuti ndikamtengere mwana wamwamuna wake mwana wa mkazi wa mphwake wa mbuyanga.
Taonani, Rebeka ali pamaso pako, mtenge ndi kumuka, akhale mkazi wa mwana wa mbuyako, monga wanena Yehova.
Ndipo Davide anati kwa khamu lonse, Mulemekeze tsono Yehova Mulungu wanu. Ndi khamu lonse linalemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao, nawerama, nalambira Yehova, ndi mfumu.
Ndipo Yehosafati anawerama mutu wake, nkhope yake pansi; ndi Ayuda onse, ndi okhala mu Yerusalemu anagwa pansi pamaso pa Yehova, nalambira Yehova.
Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Maria amake, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golide ndi lubani ndi mure.
chifukwa chake inenso ndinampereka kwa Yehova; masiku onse a moyo wake aperekedwa kwa Yehova. Ndipo analambira Yehova pomwepo.