sindiyenera zazing'ono za zifundo zonse, ndi zoona zonse, zimene mwamchitira kapolo wanu: chifukwa ndindodo yanga ndinaoloka pa Yordani uyu; ndipo tsopano ndili makamu awiri.
Genesis 24:49 - Buku Lopatulika Tsopano, ngati mudzamchitira mbuyanga zaufulu ndi zoonadi, mundiuze, ngati iai, mundiuze; kuti ndipatukire ku dzanja lamanja kapena ku dzanja lamanzere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsopano, ngati mudzamchitira mbuyanga zaufulu ndi zoonadi, mundiuze, ngati iai, mundiuze; kuti ndipatukire ku dzanja lamanja kapena ku dzanja lamanzere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsopano inu ngati muti mumkomere mtima mbuyanga mokhulupirika, chonde uzeni ndimve. Apo ai, nenaninso, kuti ine ndidziŵe chochita.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono ngati mukufuna kuonetsa kukoma mtima kwanu kwa mbuye wanga, ndikuonetsa kukhulupirika kwanu, ndiwuzeni; ndipo ngati si choncho ndiwuzeninso kuti ndidziwe chochita.” |
sindiyenera zazing'ono za zifundo zonse, ndi zoona zonse, zimene mwamchitira kapolo wanu: chifukwa ndindodo yanga ndinaoloka pa Yordani uyu; ndipo tsopano ndili makamu awiri.
Ndipo nthawi inayandikira kuti Israele adzafa, ndipo anaitana Yosefe mwana wake wamwamuna, nati kwa iye, Ngati ndapeza ufulu pamaso pako, ikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga, nundichitire ine zabwino ndi zoona: usandiikatu ine mu Ejipito;
Tipitetu pakati padziko lanu; sitidzapitira pamunda, kapena munda wampesa, sitidzamwa madzi a m'zitsime; tidzatsata mseu wachifumu; sitidzapatukira kulamanja kapena kulamanzere, mpaka titapitirira malire anu.
Ndipitire m'dziko mwako; ndidzatsata mseu, osapatuka ine ku dzanja lamanja kapena kulamanzere,
Ndipo amunawo anati kwa iye, Moyo wathu ndiwo moyo wanu, mukapanda kuwulula chodzera ife; ndipo kudzakhala kuti, pakutipatsa ife dziko ili Yehova, tidzakuchitira chifundo ndi choonadi.