Ndipo panali zitatha kumwa ngamira, munthuyo anatenga mphete yagolide ya kulemera kwake sekeli latheka, ndi zingwinjiri ziwiri za m'manja ake, kulemera kwake masekeli khumi a golide.
Genesis 24:23 - Buku Lopatulika Ndipo anati, Ndiwe mwana wa yani? Undiuzetu. Kodi kunyumba ya atate wako kuli malo akuti tigoneko ife? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati, Ndiwe mwana wa yani? Undiuzetu. Kodi kunyumba ya atate wako kuli malo akuti tigoneko ife? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka adafunsa namwaliyo kuti, “Kodi atate anu ndani? Tandiwuzani chonde. Kodi alipo malo oti ine ndi anzangaŵa nkugonako usiku uno?” Namwaliyo adayankha kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka anafunsa namwaliyo kuti, “Chonde tandiwuza, kodi ndiwe mwana wa yani? Ndipo kodi malo alipo kwanu woti ife nʼkugona?” |
Ndipo panali zitatha kumwa ngamira, munthuyo anatenga mphete yagolide ya kulemera kwake sekeli latheka, ndi zingwinjiri ziwiri za m'manja ake, kulemera kwake masekeli khumi a golide.
Ndipo mkaziyo anati kwa iye, Ine ndine mwana wa Betuele mwana wamwamuna wa Milika, amene anambalira Nahori.
Ndipo ndinamfunsa iye kuti, Ndiwe mwana wa yani kodi? Ndipo anati, Ndine mwana wa Betuele, mwana wa Nahori amene anambalira iye Milika: ndipo ndinaika mphete pambuyo pake ndi zingwinjiri pa manja ake.