Genesis 24:20 - Buku Lopatulika Ndipo anafulumira nathira madzi a m'mtsuko wake m'chomwera, nathamangiranso kuchitsime kukatunga, nazitungira ngamira zake zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anafulumira nathira madzi a m'mtsuko wake m'chomwera, nathamangiranso kuchitsime kukatunga, nazitungira ngamira zake zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pompo madzi amumtsukowo adaŵatsanyulira m'chomwera nyama, nabwerera ku chitsime kukatenga madzi ena oti amwetse ngamirazo mpaka zitakwana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho anafulumira kukhuthula madzi a mu mtsuko aja momwera ziweto, nathamanga kubwerera ku chitsime kukatunga madzi ena, ndipo anatunga okwanira ngamira zake zonse. |
Munthuyo ndipo anamyang'anira iye, nakhala chete, kuti adziwe ngati Yehova anamuyendetsa bwino kapena iai.
Ndipo anadalitsa Yosefe, nati, Mulungu, pamaso pake anayenda makolo anga Abrahamu ndi Isaki, Mulungu amene anandidyetsa ine nthawi zonse za moyo wanga kufikira lero,