Ndisanathe kunena m'mtima mwanga, taonani, Rebeka anatuluka ndi mtsuko wake pa phewa lake, natsikira ku kasupe, natunga: ndipo ndinati kwa iye, Ndimwetu.
Genesis 24:17 - Buku Lopatulika Ndipo mnyamatayo anamthamangira kukomana naye, nati, Ndimwetu madzi pang'ono a m'mtsuko mwako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mnyamatayo anamthamangira kukomana naye, nati, Ndimwetu madzi pang'ono a m'mtsuko mwako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono wantchito uja adamthamangira kuti akakumane naye, nampempha kuti, “Chonde mundipatseko madzi a mumtsuko mwanu kuti ndimwe.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wantchito uja anathamanga kukakumana naye nati, “Chonde patseko madzi pangʼono a mu mtsuko wakowo kuti ndimwe.” |
Ndisanathe kunena m'mtima mwanga, taonani, Rebeka anatuluka ndi mtsuko wake pa phewa lake, natsikira ku kasupe, natunga: ndipo ndinati kwa iye, Ndimwetu.
Tsono iye ananyamuka nanka ku Zarefati, nafika ku chipata cha mzinda; ndipo taona mkazi wamasiye anali kutola nkhuni; ndipo iye anamuitana, nati, Unditengere madzi pang'ono m'chikho, ndimwe.
Muchingamire akumva ludzu ndi madzi; okhala m'dziko la Tema ananka kukomana ndi othawa ndi chakudya chao.
Ndipo pamwamba pa mapiri aakulu onse, ndi pa zitunda zonse zazitalitali padzakhala mitsinje ndi micherenje ya madzi, tsiku lophana lalikulu, pamene nsanja zidzagwa.
Iwo sadzakhala ndi njala, pena ludzu; ngakhale thukuta, pena dzuwa silidzawatentha; pakuti Iye amene wawachitira chifundo, adzawatsogolera, ngakhale pa akasupe a madzi adzawatsogolera.
Kunali ngati ora lachisanu ndi chimodzi. Kunadza mkazi wotuluka mu Samariya kudzatunga madzi. Yesu ananena naye, Undipatse Ine ndimwe.
Pamenepo mkazi wa mu Samariya ananena ndi Iye, Bwanji Inu, muli Myuda, mupempha kwa ine kumwa, ndine mkazi Msamariya? (Pakuti Ayuda sayenderana nao Asamariya).