Ndipo ana a Hiti analimbitsira Abrahamu munda, ndi phanga lili m'menemo, likhale lake lamanda.
Genesis 23:17 - Buku Lopatulika Ndipo munda wa Efuroni umene unali mu Makipela, umene unali patsogolo pa Mamure, munda ndi phanga lili momwemo, ndi mitengo yonse inali m'mundamo, yokhala m'malire monse mozungulira momwemo, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo munda wa Efuroni umene unali m'Makipela, umene unali patsogolo pa Mamure, munda ndi phanga lili momwemo, ndi mitengo yonse inali m'mundamo, yokhala m'malire monse mozungulira momwemo, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Umu ndimo m'mene kadziko kaja ka Efuroni ka ku Makipera, kuvuma kwa Mamure, kadasandukira ka Abrahamu. Panali munda ndi phanga lokhala m'malire mwa mundawo, pamodzi ndi mitengo yonse yam'mundamo mpaka kukalekeza ku malire ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho munda wa Efroni wa ku Makipela umene unali kufupi ndi Mamre, kuphatikiza munda, phanga linali mʼmenemo pamodzi ndi mitengo yonse ya mʼmundamo, zinaperekedwa |
Ndipo ana a Hiti analimbitsira Abrahamu munda, ndi phanga lili m'menemo, likhale lake lamanda.
munda umene anagula Abrahamu kwa ana a Hiti. Pamenepo anamuika Abrahamu ndi Sara mkazi wake.
Ndipo ana ake Isaki ndi Ismaele anamuika iye m'phanga la Makipela, m'munda wa Efuroni mwana wake wa Zohari Muhiti, umene uli patsogolo pa Mamure;
koma pamene ndidzagona ndi makolo anga, udzanditenge ine kutuluka m'dziko la Ejipito, ukandiike ine m'manda mwao. Ndipo iye anati, Ndidzachita monga mwanena.
chifukwa kuti ana ake aamuna anamnyamula iye kulowa naye m'dziko la Kanani, ndi kumuika iye m'phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula pamodzi ndi munda, likhale poikira pake, kwa Efuroni Muhiti, patsogolo pa Mamure.
Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa; adzalimbika nao mlandu wake poweruzidwa.
Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.
ndipo anawanyamula kupita nao ku Sekemu, nawaika m'manda amene Abrahamu adagula ndi mtengo wake wa ndalama kwa ana a Hamori mu Sekemu.