Genesis 23:15 - Buku Lopatulika Mfumu, mundimvere ine; kadziko ka mtengo wake wa masekeli a siliva mazana anai, ndiko chiyani pakati pa ine ndi inu? Ikani wakufa wanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mfumu, mundimvere ine; kadziko ka mtengo wake wa masekeli a siliva mazana anai, ndiko chiyani pakati pa ine ndi inu? Ikani wakufa wanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Mvereni, mbuyanga. Malowo mtengo wake ndi masekeli a siliva okwana 400. Koma zimenezo nchiyani pakati pa inu ndi ine? Ikani maliro anu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Mundimvere mbuye wanga; mundawo mtengo wake ndi masekeli asiliva okwana 400. Koma zimenezo nʼchiyani pakati pa ine ndi inu? Ikani mtembo wa mkazi wanu.” |
Ndipo anagula ndi ndalama zana limodzi dera la munda kumeneko anamanga hema wake, padzanja la ana ake a Hamori atate wake wa Sekemu.
Ichi achipereke, yense wakupita kwa owerengedwa; limodzi la magawo awiri a sekeli, monga sekeli la malo opatulika; (sekeli ndilo magera makumi awiri,) limodzi la magawo awiri a sekeli, ndilo chopereka cha Yehova.
Wachuma asachulukitsepo, ndi osauka asachepse pa limodzi mwa magawo awiri a sekeli, pakupereka chopereka kwa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu.
Ndipo sekeli ndilo magera makumi awiri; masekeli makumi awiri, ndi masekeli awiri ndi asanu, ndi masekeli khumi ndi asanu, ndiwo muyeso wa mina wanu.