Ndipo panali zitapita izi, anauza Abrahamu kuti, Taonani, Milika iyenso anambalira Nahori mphwako ana;
Genesis 22:21 - Buku Lopatulika Uzi woyamba ndi Buzi mphwake, ndi Kemuwele atate wake wa Aramu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Uzi woyamba ndi Buzi mphwake, ndi Kemuwele atate wake wa Aramu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwana wake wachisamba anali Uzi, mng'ono wa Uziyo anali Buzi. Panalinso Kemuwele, bambo wake wa Aramu, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Woyamba anali Huzi ndipo kenaka mʼbale wake Buzi. Anaberekanso Kemueli, amene anali abambo ake a Aramu. |
Ndipo panali zitapita izi, anauza Abrahamu kuti, Taonani, Milika iyenso anambalira Nahori mphwako ana;
Ndipo mnyamatayo anatenga ngamira khumi za mbuyake, namuka: chifukwa kuti chuma chonse cha mbuyake chinali m'dzanja lake: ndipo anachoka namuka ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori.
Panali munthu m'dziko la Uzi, dzina lake ndiye Yobu; ndipo munthuyu anali wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.
Ndipo adapsa mtima Elihu mwana wa Barakele wa ku Buzi, wa chibale cha Ramu, adapsa mtima pa Yobu; pakuti anadziyesera yekha wolungama, wosati Mulungu.
ndi anthu onse osakanizidwa, ndi mafumu onse a dziko la Uzi, ndi mafumu onse a dziko la Afilisti, ndi Asikeloni, ndi Gaza, ndi Ekeroni, ndi otsala a Asidodi,
Ndipo ananena fanizo lake, nati, Ku Aramu ananditenga Balaki, mfumu ya Mowabu ananditenga ku mapiri a kum'mawa, Idza, udzanditembererere Yakobo. Idza, nudzanyoze Israele.