Ndipo Tera anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi awiri, nabala Abramu, ndi Nahori ndi Harani.
Genesis 22:20 - Buku Lopatulika Ndipo panali zitapita izi, anauza Abrahamu kuti, Taonani, Milika iyenso anambalira Nahori mphwako ana; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali zitapita izi, anauza Abrahamu kuti, Taonani, Milika iyenso anambalira Nahori mphwako ana; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Abrahamu adamva kuti Milika adabalira Nahori mbale wake ana asanu ndi atatu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Patapita nthawi, Abrahamu anamva kuti, “Milika nayenso anaberekera Nahori, mʼbale wake ana. |
Ndipo Tera anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi awiri, nabala Abramu, ndi Nahori ndi Harani.
Mibadwo ya Tera ndi iyi: Tera anabala Abramu, ndi Nahori, ndi Harani; ndipo Harani anabala Loti.
Ndipo Abramu ndi Nahori, anadzitengera okha akazi; dzina lake la mkazi wa Abramu ndilo Sarai; ndi dzina lake la mkazi wa Nahori ndilo Milika, mwana wake wa Harani, atate wake wa Milika, ndi atate wake wa Isika.
Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.
Ndipo mnyamatayo anatenga ngamira khumi za mbuyake, namuka: chifukwa kuti chuma chonse cha mbuyake chinali m'dzanja lake: ndipo anachoka namuka ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori.
Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anatuluka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwake wa Abrahamu, ndi mtsuko wake paphewa pake.
Ndipo mkaziyo anati kwa iye, Ine ndine mwana wa Betuele mwana wamwamuna wa Milika, amene anambalira Nahori.
Mulungu wa Abrahamu ndi Mulungu wa Nahori, Mulungu wa atate wao aweruze pa ife. Ndipo Yakobo analumbirira pa Kuopsa kwa atate wake Isaki.