Ndipo Abrahamu anatukula maso ake nayang'ana taonani, pambuyo pake nkhosa yamphongo yogwiridwa ndi nyanga zake m'chiyangoyangomo; ndipo ananka Abrahamu nakatenga nkhosa yamphongoyo, naipereka nsembe yopsereza m'malo mwa mwana wake.
Genesis 22:14 - Buku Lopatulika Ndipo Abrahamu anatcha dzina lake la malowo Yehova-Yire: monga ati lero lomwe, M'phiri la Yehova chidzaoneka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abrahamu anatcha dzina lake la malowo Yehova-Yire: monga ati lero lomwe, M'phiri la Yehova chidzaoneka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abrahamu adaŵatcha malowo kuti Chauta adapatsa. Ndipo mpaka lero lino anthu amati, “Paphiri la Chauta adzapatsa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Abrahamu anatcha malo amenewa kuti Yehova-Yire (Wopereka). Ndipo mpaka lero amatchula malowo kuti ndi “Pa phiri la Yehova wopereka.” |
Ndipo Abrahamu anatukula maso ake nayang'ana taonani, pambuyo pake nkhosa yamphongo yogwiridwa ndi nyanga zake m'chiyangoyangomo; ndipo ananka Abrahamu nakatenga nkhosa yamphongoyo, naipereka nsembe yopsereza m'malo mwa mwana wake.
Ndipo Abrahamu anati, Mwana wanga, Mulungu adzadzifunira yekha mwanawankhosa wa nsembe yopsereza; nayenda pamodzi onse awiri.
Ndipo Yakobo anatcha dzina la malo amenewo, Penuwele: chifukwa ndaonana ndi Mulungu nkhope ndi nkhope, ndipo wapulumuka moyo wanga.
Pozungulira pake ndipo mikono zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi dzina la mzindawo kuyambira tsiku ilo lidzakhala, Yehova ali pomwepo.
Imva zowawa, nuyesetse kubala, mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mkazi wakubala; pakuti udzatuluka m'mzinda tsopano, nudzakhala kuthengo, nudzafika ku Babiloni; komweko udzapulumutsidwa; komweko Yehova adzakuombola m'manja a adani ako.
Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.
Popeza Yehova adzaweruza anthu ake, nadzachitira nsoni anthu ake; pakuona Iye kuti mphamvu yao yatha, wosatsala womangika kapena waufulu.
Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.
Pamenepo Gideoni anammangira Yehova guwa la nsembe pomwepo; nalitcha Yehova-ndiye-mtendere; likali mu Ofura wa Aabiyezere ndi pano pomwe.
Chifukwa chake ulawirire m'mawa pamodzi ndi anyamata a mbuye wako amene anabwera nawe; ndipo mutauka m'mawa, mumuke kutacha.
Pamenepo Samuele anatenga mwala nauimika pakati pa Mizipa ndi Sene, nautcha dzina lake Ebenezeri, nati, Kufikira pano Yehova anatithandiza.