Abrahamu ndipo anachoka kumeneko kunka ku dziko la kumwera, ndipo anakhala pakati pa Kadesi ndi Suri, ndipo anakhala ngati mlendo mu Gerari.
Genesis 21:34 - Buku Lopatulika Ndipo Abrahamu anakhala ngati mlendo masiku ambiri m'dziko la Afilisti. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abrahamu anakhala ngati mlendo masiku ambiri m'dziko la Afilisti. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo adakhala m'dziko la Afilisti nthaŵi yaitali. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Abrahamu anakhala mʼdziko la Afilisti kwa nthawi yayitali. |
Abrahamu ndipo anachoka kumeneko kunka ku dziko la kumwera, ndipo anakhala pakati pa Kadesi ndi Suri, ndipo anakhala ngati mlendo mu Gerari.
Ndipo Abrahamu anabwera kwa anyamata ake, ndipo anauka nayenda pamodzi kumuka ku Beereseba; ndipo anakhala Abrahamu pa Beereseba.
Pakuti ife ndife alendo pamaso panu, ndi ogonera, monga makolo athu onse; masiku athu a padziko akunga mthunzi, ndipo palibe kukhalitsa.
Imvani pemphero langa, Yehova, ndipo tcherani khutu kulira kwanga; musakhale chete pa misozi yanga; Pakuti ine ndine mlendo ndi Inu, wosakhazikika, monga makolo anga onse.
Iwo onse adamwalira m'chikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali, navomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.
Ndi chikhulupiriro anakhala mlendo kudziko la lonjezano, losati lake, nakhalira m'mahema pamodzi ndi Isaki ndi Yakobo, olowa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwelo;
Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo;