Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 21:32 - Buku Lopatulika

Ndipo anapangana pangano pa Beereseba: ndipo anauka Abimeleki ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yake, nabwera kunka ku dziko la Afilisti.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anapangana pangano pa Beereseba: ndipo anauka Abimeleki ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yake, nabwera kunka ku dziko la Afilisti.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Atachita chipangano chimenechi ku Beereseba kuja, Abimeleki ndi Fikolo mkulu wa gulu la ankhondo, adabwerera kwao ku dziko la Afilisti.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Atatha kuchita pangano pa Beeriseba, Abimeleki ndi Fikolo mkulu wankhondo wake anabwerera ku dziko la Afilisti.

Onani mutuwo



Genesis 21:32
12 Mawu Ofanana  

ndi Patirusimu, ndi Kasiluhimu, m'menemo ndipo anatuluka Afilisti, ndi Kafitori.


Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Muhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure Mwamori, mkulu wake wa Esikolo, ndi mkulu wake wa Anere; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.


Ndipo Abrahamu anatenga nkhosa ndi ng'ombe, nampatsa Abimeleki, ndipo anapangana pangano onse awiriwo.


Chifukwa chake anatcha malowo Beereseba: chifukwa pamenepo analumbira onse awiri.


Ndipo Abrahamu anaoka mtengo wa bwemba pa Beereseba, naitanira pamenepo dzina la Yehova, Mulungu wa nthawi zonse.


ndipo anali ndi chuma cha nkhosa, ndi chuma cha zoweta, ndi banja lalikulu: ndipo Afilisti anamchitira iye nsanje.


Ndipo panali atakhala komwe masiku ambiri, Abimeleki mfumu ya Afilisti, anayang'ana kunja kwa zenera, napenya, taona, Isaki analinkuseka ndi Rebeka mkazi wake.


Tsopano tiyeni tipangane pangano, ine ndi iwe; likhale mboni pakati pa ine ndi iwe.


Mulungu wa Abrahamu ndi Mulungu wa Nahori, Mulungu wa atate wao aweruze pa ife. Ndipo Yakobo analumbirira pa Kuopsa kwa atate wake Isaki.


Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolere njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati, Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m'mbuyo kunka ku Ejipito.


Ndipo ana a Israele anaonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova; nawapereka Yehova m'dzanja la Afilisti zaka makumi anai.


Pamenepo Yonatani ndi Davide anapangana pangano, pakuti adamkonda iye ngati moyo wa iye yekha.