Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Muhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure Mwamori, mkulu wake wa Esikolo, ndi mkulu wake wa Anere; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.
Genesis 21:27 - Buku Lopatulika Ndipo Abrahamu anatenga nkhosa ndi ng'ombe, nampatsa Abimeleki, ndipo anapangana pangano onse awiriwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abrahamu anatenga nkhosa ndi ng'ombe, nampatsa Abimeleki, ndipo anapangana pangano onse awiriwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abrahamu adapatsa Abimeleki nkhosa ndi ng'ombe, ndipo onse aŵiriwo adachita chipangano. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Abrahamu anabweretsa nkhosa ndi ngʼombe nazipereka kwa Abimeleki, ndipo anthu awiriwo anachita pangano. |
Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Muhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure Mwamori, mkulu wake wa Esikolo, ndi mkulu wake wa Anere; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.
Ndipo anati Abimeleki, Sindinadziwe amene anachita icho; ndipo iwe sunandiuze ine, ndiponso sindinamve koma lero lino.
ndipo inatenga wa mbumba yachifumu, nkuchita naye pangano, nkumlumbiritsa, nkuchotsa amphamvu a m'dziko;
Abale, ndinena monga munthu. Pangano, lingakhale la munthu, litalunzika, palibe munthu aliyesa chabe, kapena kuonjezapo.
Pamenepo Yonatani ndi Davide anapangana pangano, pakuti adamkonda iye ngati moyo wa iye yekha.