Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Muhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure Mwamori, mkulu wake wa Esikolo, ndi mkulu wake wa Anere; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.
Genesis 21:24 - Buku Lopatulika Ndipo Abrahamu anati, Ine ndidzalumbira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abrahamu anati, Ine ndidzalumbira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abrahamu adati, “Ndikulumbira.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abrahamu anati, “Ine ndikulumbira.” |
Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Muhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure Mwamori, mkulu wake wa Esikolo, ndi mkulu wake wa Anere; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.
tsopano iwe undilumbirire ine pano pa Mulungu kuti sudzandinyenga ine, kapena mwana wanga, kapena mdzukulu wanga: koma monga ufulu ndakuchitira iwe udzandichitire ine, ndi dziko lomwe wakhalamo, ngati mlendo.
Ndipo Abrahamu anamdzudzula Abimeleki chifukwa cha chitsime cha madzi, anyamata ake a Abimeleki anachilanda.
Ndipo anati, Undilumbirire ine; namlumbirira iye. Ndipo Israele anawerama kumutu kwa kama.
Pakuti anthu amalumbira pa wamkulu; ndipo m'chitsutsano chao chilichonse lumbiro litsiriza kutsimikiza.