Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ndidzachulukitsa ndithu mbeu zako, kuti unyinji wao sudzawerengeka.
Genesis 21:13 - Buku Lopatulika Ndipo mwana wamwamuna wa mdzakazi uyo ndidzayesa mtundu, chifukwa iye ndiye mbeu yako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mwana wamwamuna wa mdzakazi uyo ndidzayesa mtundu, chifukwa iye ndiye mbeu yako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwana wa mdzakaziyunso ndidzampatsa ana ambiri, ndipo adzasanduka mtundu ndithu, popeza kuti iyeyunso ndi mwana wako.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwana wa mdzakazi wakoyu ndidzamusandutsa mtundu wa anthu chifukwa ndi mwana wako.” |
Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ndidzachulukitsa ndithu mbeu zako, kuti unyinji wao sudzawerengeka.
Koma za Ismaele, ndamvera iwe: taona, ndamdalitsa iye, ndipo ndidzamchulukitsa iye ndithu; adzabala akalonga khumi ndi awiri, ndipo ndidzamuyesa iye mtundu waukulu.
Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi thumba la madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.
Tauka, nuukitse mnyamatayo, ndi kumgwira m'dzanja lako; chifukwa ndidzamuyesa iye mtundu waukulu.