Ndipo anamchitira Abramu bwino chifukwa cha iyeyo; ndipo anali nazo nkhosa, ndi ng'ombe, ndi abulu, ndi akapolo, ndi adzakazi, ndi abulu aakazi, ndi ngamira.
Genesis 20:14 - Buku Lopatulika Ndipo Abimeleki anatenga nkhosa ndi ng'ombe ndi akapolo ndi adzakazi nampatsa Abrahamu, nambwezera iye Sara mkazi wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abimeleki anatenga nkhosa ndi ng'ombe ndi akapolo ndi adzakazi nampatsa Abrahamu, nambwezera iye Sara mkazi wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Abimeleki adabwezera Sara kwa Abrahamu, ndipo nthaŵi yomweyo adampatsa nkhosa, ng'ombe ndi akapolo aamuna ndi aakazi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Abimeleki anapereka nkhosa, ngʼombe ndi antchito aamuna ndi aakazi kwa Abrahamu. Ndipo anamubwezeranso Abrahamu Sara, mkazi wake. |
Ndipo anamchitira Abramu bwino chifukwa cha iyeyo; ndipo anali nazo nkhosa, ndi ng'ombe, ndi abulu, ndi akapolo, ndi adzakazi, ndi abulu aakazi, ndi ngamira.
Ndipo Abrahamu anati, Chifukwa ndinati, Pompano palibe ndithu kumuopa Mulungu, ndipo adzandipha ine chifukwa cha mkazi wanga.
Ndipo Abrahamu anati za Sara mkazi wake, Iye ndiye mlongo wanga: ndipo Abimeleki mfumu ya Gerari anatumiza namtenga Sara
Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wake; chifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao.
Ndipo panali nthawi yomweyo, Abimeleki ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yake anati kwa Abrahamu, kuti, Mulungu ali pamodzi ndi iwe m'zonse uzichita iwe;
Koma kapolo uyo akanena mumtima mwake, Mbuye wanga azengereza kudza; ndimo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi ndi kudya ndi kumwa, ndi kuledzera;