Ndipo Yehova anati kwa Abramu, Tuluka iwe m'dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi kunyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe;
Genesis 20:13 - Buku Lopatulika Ndipo panali pamene Mulungu anandiyendetsa ine kunyumba kwa atate wanga, ndinati kwa mkaziyo, Ichi ndicho chokoma mtima udzandichitire ine, konse kumene tidzafika ife, uzinena za ine, Iye ndiye mlongo wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali pamene Mulungu anandiyendetsa ine kunyumba kwa atate wanga, ndinati kwa mkaziyo, Ichi ndicho chokoma mtima udzandichitire ine, konse kumene tidzafika ife, uzinena za ine, Iye ndiye mlongo wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero pamene Mulungu adandituma kuchokera kunyumba kwa bambo wanga, kuti ndipite ku maiko achilendo, ndidaamuuza mkazi wangayu kuti, ‘Undiwonetse kuti ndiwedi wokhulupirika kwa ine, pouza aliyense kuti ndine mlongo wako, kulikonse kumene tizipita.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndiye pamene Mulungu anati ndichoke ku nyumba ya abambo anga, ndinawuza mkazi wangayu kuti, ‘Kuti uwonetse kuti ndiwe mkazi wokoma mtima, uziwuza anthu kulikonse kumene tingapite kuti ndine mlongo wako.’ ” |
Ndipo Yehova anati kwa Abramu, Tuluka iwe m'dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi kunyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe;
Koma ndiye mlongo wanga ndithu, mwana wa atate wanga, koma si mwana wa amai wanga: ndipo anakhala ndi ine mkazi wanga.
Kodi iye sanati kwa ine, Ndiye mlongo wanga: ndipo mkazi iye yekha anati, Iye ndiye mlongo wanga: ndi mtima wanga wangwiro ndi manja anga osachimwa ndachita ine ichi.
Alimbikitsana m'chinthu choipa; apangana za kutchera misampha mobisika; akuti, Adzaiona ndani?
Koma Petro anati kwa iye, Munapangana pamodzi bwanji kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona, mapazi ao a iwo amene anaika mwamuna wako ali pakhomo, ndipo adzakunyamula kutuluka nawe.
Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka kumalo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako.