Koma asanagone, anthu a m'mzindamo anthu a Sodomu, anazinga nyumba, anyamata ndi okalamba, anthu onse a m'mbali zonse;
Genesis 19:7 - Buku Lopatulika Ndipo anati, Abale anga, musachitetu koipa kotere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati, Abale anga, musachitetu koipa kotere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adaŵapempha kuti, “Inu abwenzi anga, musachite zimenezi chifukwa nkulakwa kwambiri kuchita zotere. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anati, “Ayi anzanga, musachite zinthu zoyipa zotere. |
Koma asanagone, anthu a m'mzindamo anthu a Sodomu, anazinga nyumba, anyamata ndi okalamba, anthu onse a m'mbali zonse;
Taonanitu, ndili ndi ana aakazi awiri, amene sanadziwe mwamuna; ndiwatulutsire iwo kwa inu, muchite nao chomwe chikomera inu; koma anthu awa musawachitire iwo kanthu; chifukwa kuti anadza iwo pansi pa mthunzi wa tsindwi langa.
Munthu akagonana ndi mwamuna mnzake, monga amagonana ndi mkazi, achita chonyansa onse awiri; awaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamutu pao.
ndipo ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zao, ndi malekezero a pokhala pao;
Chifukwa chake Mulungu anawapereka iwo m'zilakolako za mitima yao, kuzonyansa, kuchititsana matupi ao wina ndi mnzake zamanyazi;
Pasakhale mkazi wachigololo pakati pa ana aakazi a Israele, kapena wachigololo pakati pa ana aamuna a Israele.
Monga Sodomu ndi Gomora, ndi mizinda yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kutsata zilakolako zachilendo, iikidwa chitsanzo, pakuchitidwa chilango cha moto wosatha.
Ndipo munthu mwini nyumba anawatulukira nanena nao, Iai, abale anga, musachite choipa chotere; popeza mwamuna uyu walowa m'nyumba mwanga, musachite chopusa ichi.
Ndipo Gaala, mwana wa Ebedi anadza ndi abale ake, napita ku Sekemu; ndi eni ake a ku Sekemu anamkhulupirira.