Ndipo anamwetsa vinyo atate wao usiku womwenso; wamng'ono ndipo anauka nagona naye; ndipo iye sanadziwe pomwe anagona ndi pomwe anauka.
Genesis 19:36 - Buku Lopatulika Ndipo ana aakazi awiri a Loti anali ndi pakati pa atate wao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ana akazi awiri a Loti anali ndi pakati pa atate wao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwa njira imeneyi, ana onse aŵiriwo a Loti adatenga pathupi pa bambo wao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho ana onse awiri a Loti aja anatenga pathupi pa abambo awo. |
Ndipo anamwetsa vinyo atate wao usiku womwenso; wamng'ono ndipo anauka nagona naye; ndipo iye sanadziwe pomwe anagona ndi pomwe anauka.
Woyamba ndipo anabala mwana wamwamuna, namtcha dzina lake. Mowabu; yemweyo ndi atate wa Amowabu kufikira lero.
Taonanitu, ndili ndi ana aakazi awiri, amene sanadziwe mwamuna; ndiwatulutsire iwo kwa inu, muchite nao chomwe chikomera inu; koma anthu awa musawachitire iwo kanthu; chifukwa kuti anadza iwo pansi pa mthunzi wa tsindwi langa.
Tsoka wakuninkha mnzake chakumwa, ndi kuonjezako mankhwala ako, ndi kumledzeretsa, kuti upenyerere manyazi ao!
Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso.
Ndipo Yehova anati kwa ine, Usavuta Mowabu, kapena kuutsana naye nkhondo; popeza sindidzakupatsako dziko lake likhale lakolako; pakuti ndinapatsa ana a Loti Ari likhale laolao.
Pamenepo anati Adoni-Bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikulu za m'manja ndi m'mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinachita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye ku Yerusalemu, nafa iye komweko.
Ndipo Samuele anati, Monga lupanga lako linachititsa akazi ufedwa, momwemo mai wako adzakhala mfedwa mwa akazi. Ndipo Samuele anamdula Agagi nthulinthuli pamaso pa Yehova ku Giligala.