Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziotchetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope.
Genesis 19:32 - Buku Lopatulika tiyeni, timwetse atate vinyo, tidzagona naye, kuti tisunge mbeu za atate wathu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 tiyeni, timwetse atate vinyo, tidzagona naye, kuti tisunge mbeu za atate wathu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tiye tiŵaledzeretse abamboŵa kuti agone nafe, kuti mtundu usathe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tiye tiwamwetse vinyo ndipo tigone nawo. Tikatero mtundu wathu udzakhalapobe.” |
Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziotchetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope.
Ndipo anamwetsa atate wao vinyo usiku womwewo; woyamba ndipo analowa nagona naye atate wake; ndipo sanadziwe pomwe anagona ndi pomwe anauka.
Mphunzitsi, Mose anatilembera, kuti, Akafa mbale wake wa munthu, nasiya mkazi, wosasiya mwana, mbale wake atenge mkazi wake, namuukitsire mbale wakeyo mbeu.
Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha;