Ndipo panali pamene anawatulutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa paliponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke.
Genesis 19:26 - Buku Lopatulika Koma mkazi wake anacheuka ali pambuyo pake pa Loti, nasanduka mwala wamchere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma mkazi wake anacheuka ali pambuyo pake pa Loti, nasanduka mwala wamchere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma mkazi wa Loti adaacheukira m'mbuyo, ndiye pomwepo adasanduka mwala wamchere. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma mkazi wa Loti anachewuka ndipo anasanduka mwala wa mchere. |
Ndipo panali pamene anawatulutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa paliponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke.
Wobwerera m'mbuyo m'mtima adzakhuta njira yake; koma munthu wabwino adzakhuta za mwa iye yekha.
mbale zofukizazo za iwo amene adachimwira moyo waowao, ndipo azisule zaphanthiphanthi, zikhale chivundikiro cha guwa la nsembe; popeza anabwera nazo pamaso pa Yehova, chifukwa chake zikhala zopatulika; ndipo zidzakhala chizindikiro kwa ana a Israele.
Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo wochokera m'chikhulupiriro: Ndipo ngati abwerera, moyo wanga ulibe kukondwera mwa iye.