Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 19:20 - Buku Lopatulika

taonanitu, mzinda uwu uli pafupi pothawirapo, ndipo uli waung'ono; ndithawiretu kumeneko, suli waung'ono nanga? Ndipo ndidzakhala ndi moyo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

taonanitu, mudzi uwu uli pafupi pothawirapo, ndipo uli waung'ono; ndithawiretu kumeneko, suli waung'ono nanga? Ndipo ndidzakhala ndi moyo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Apo patsidyapo pali kamzinda kakang'ono. Pamenepo mpafupi, ndingathe kukafika. Bwanji ndipite kumeneko. Nkochepa kwambiri, koma ndikhoza kupulumukirako.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma, chapafupi pomwepa pali mudzi woti ndikhoza kuthamanga nʼkukafikako. Mundilole ndithawireko, ndi waungʼono kwambiri, si choncho? Mukatero, moyo wanga upulumuka.”

Onani mutuwo



Genesis 19:20
9 Mawu Ofanana  

Uzikanenatu, kuti iwe ndiwe mlongo wanga: kuti chidzakhala chabwino ndi ine, chifukwa cha iwe, ndi kuti moyo wanga usungike ndi iwe.


taonanitu, kapolo wanu anapeza ufulu pamaso panu, ndipo munakuza chifundo chanu, chimene munandichitira ine, pakupulumutsa moyo wanga; ine sindikhoza kuthawira kuphiri kuti chingandipeze ine choipacho ndingafe;


Ndipo anati kwa iye, Taona, ndikuvomereza iwe pamenepanso kuti sindidzaononga mzinda uwu umene wandiuza.


Ndipo Loti anabwera kutuluka mu Zowari nakhala m'phiri ndi ana aakazi awiri pamodzi naye: chifukwa anaopa kukhala mu Zowari, ndipo anakhala m'phanga, iye ndi ana ake aakazi.


Mzimu wanga ukhale ndi moyo, ndipo udzakulemekezani; ndipo maweruzo anu andithandize.


Tcherani khutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanu chipangano chosatha, ndicho zifundo zoona za Davide.


Koma Yeremiya anati, Sadzakuperekani. Mveranitu mau a Yehova, amene ndinena ndi inu, chomwecho kudzakomera inu, ndipo moyo wanu udzakhalabe.


Kodi adzaomba lipenga m'mzinda osanjenjemera anthu? Kodi choipa chidzagwera mzinda osachichita Yehova?