Pamene kunacha, amithengawo anafulumiza Loti, nati, Uka, tenga mkazi wako, ndi ana ako aakazi awiri amene ali kunowa, kuti munganyeke m'mphulupulu ya mzinda.
Genesis 19:16 - Buku Lopatulika Koma anachedwa; ndipo anthuwo anamgwira dzanja lake, ndi dzanja la mkazi wake ndi dzanja la ana ake aakazi awiri; chifukwa cha kumchitira chifundo Yehova; ndipo anamtulutsa iye, namuika kunja kwa mzinda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma anachedwa; ndipo anthuwo anamgwira dzanja lake, ndi dzanja la mkazi wake ndi dzanja la ana ake akazi awiri; chifukwa cha kumchitira chifundo Yehova; ndipo anamtulutsa iye, namuika kunja kwa mudzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Loti ankakayikabe, tsono Chauta adamumvera chifundo. Motero anthuwo adatenga Loti, mkazi wake ndi ana ake aŵiri aja moŵagwira pa dzanja, naŵatulutsa mumzindamo, nkuŵasiya panja pomwepo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Loti ankakayikabe. Koma Yehova anawachitira chifundo motero kuti anthu aja anagwira mkazi wake ndi ana ake aakazi aja nawatsogolera bwinobwino kuwatulutsa mu mzindawo. |
Pamene kunacha, amithengawo anafulumiza Loti, nati, Uka, tenga mkazi wako, ndi ana ako aakazi awiri amene ali kunowa, kuti munganyeke m'mphulupulu ya mzinda.
Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo, wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.
Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.
Ndipo Yehova anapita pamaso pake, nafuula, Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi;
wakusungira anthu osawerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula; wakulanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.
M'mazunzo ao onse Iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pake anawapulumutsa; m'kukonda kwake ndi m'chisoni chake Iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale.
Yehova ndiye wolekereza, ndi wa chifundo chochuluka, wokhululukira mphulupulu ndi kulakwa, koma wosamasula wopalamula; wakuwalanga ana chifukwa cha mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.
Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafune kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa.
Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amkoka iye; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse,
popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wachifundo; sadzakusiyani, kapena kukuonongani, kapena kuiwala chipangano cha makolo anu chimene analumbirira iwo.
Ndipo uzikumbukira kuti unali kapolo m'dziko la Ejipito, ndi kuti Yehova Mulungu wako anakutulutsako ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka; chifukwa chake Yehova Mulungu wako anakulamulira kusunga tsiku la Sabata.
Pamenepo muzinena kwa ana anu, Tinali akapolo a Farao mu Ejipito; ndipo Yehova anatitulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.
koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu, ndi kukuombolani m'nyumba ya ukapolo, m'dzanja la Farao mfumu ya Aejipito, chifukwa Yehova akukondani, ndi chifukwa cha kusunga lumbiro lija analumbirira makolo anu.
zosati zochokera m'ntchito za m'chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,
Ndipo Yoswa ananena kwa amuna awiri anazonda dzikowo, Lowani m'nyumba ya mkazi wadamayo, ndi kutulutsamo mkaziyo ndi zonse ali nazo, monga munamlumbirira iye.
Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe;