Ndipo anthu aja anati kwa Loti, Kodi muli nao ena pano? Mkamwini, ndi ana ako aamuna, ndi ana ako aakazi, ndi onse ali nao m'mzinda muno, utuluke nao m'malo muno:
Genesis 19:11 - Buku Lopatulika Ndipo anachititsa khungu m'maso mwa anthu amene anali pakhomo pa nyumba, aang'ono ndi aakulu, ndipo anavutika kufufuza pakhomo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anachititsa khungu m'maso mwa anthu amene anali pakhomo pa nyumba, ang'ono ndi akulu, ndipo anavutika kufufuza pakhomo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka adaŵachititsa khungu anthu onse amene adaaima pabwalowo, achinyamata ndi okalamba omwe, kotero kuti sadathenso kuwona khomo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka anawachititsa khungu anthu amene anali panja pa nyumba aja, aangʼono ndi aakulu omwe, kuti asaone pa khomo. |
Ndipo anthu aja anati kwa Loti, Kodi muli nao ena pano? Mkamwini, ndi ana ako aamuna, ndi ana ako aakazi, ndi onse ali nao m'mzinda muno, utuluke nao m'malo muno:
Ndipo atatsikira pali iye, Elisa anapemphera kwa Yehova, nati, Mukanthe mtundu uwu uchite khungu. Ndipo Iye anawakantha, nawachititsa khungu, monga mwa mau a Elisa.
Unatopa ndi njira yako yaitali; koma sunanene, Palibe chiyembekezo; iwe wapeza moyo wa dzanja lako; chifukwa chake sunalefuke.
Bwanji uyendayenda kwambiri ndi kusintha njira yako? Udzachitanso manyazi ndi Ejipito monga unachita manyazi ndi Asiriya.
Ndipo tsopano, taona, dzanja la Ambuye lili pa iwe, ndipo udzakhala wakhungu wosapenya dzuwa nthawi. Ndipo pomwepo lidamgwera khungu ndi mdima; ndipo anamukamuka nafuna wina womgwira dzanja.