Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanenanso: kapena akapezedwa makumi atatu m'menemo? Ndipo anati, Ndikapeza makumi atatu m'menemo sindidzachita.
Genesis 18:32 - Buku Lopatulika Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwa khumi m'menemo? Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha khumi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwa khumi m'menemo? Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha khumi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abrahamu adati, “Chonde, musandikwiyire Ambuye, koma ndilankhule kamodzi kokhaka. Nanga mutapezeka khumi okha?” Aponso Chauta adati, “Ndikapeza olungama khumi, sindidzauwononga mzindawo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Abrahamu anati, “Pepani Ambuye musandipsere mtima, ndingoyankhula kamodzi kokhaka basi. Bwanji atangopezeka khumi okha mʼmenemo?” Iye anayankha nati, “Chifukwa cha khumiwo, sindidzawuwononga.” |
Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanenanso: kapena akapezedwa makumi atatu m'menemo? Ndipo anati, Ndikapeza makumi atatu m'menemo sindidzachita.
Ndipo anati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye: kapena akapezedwa makumi awiri m'menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi awiri.
Ndipo Yuda anayandikira kwa iye nati, Mfumu, kapolo wanu aneneretu m'makutu a mbuyanga, mtima wanu usapse pokwiya ndi kapolo wanu; chifukwa muli ngati Farao.
Akakhala kwa iye mthenga, womasulira mau mmodzi mwa chikwi, kuonetsera munthu chomuyenera;
Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.
Atero Yehova, Monga vinyo watsopano apezedwa m'tsango, ndipo wina ati, Usaliononge, pakuti muli mdalitso m'menemo, ndidzachita chifukwa cha atumiki anga, kuti ndisawaononge onse.
Thamangani inu kwina ndi kwina m'miseu ya Yerusalemu, taonanitu, dziwani, ndi kufunafuna m'mabwalo ake, kapena mukapeza munthu, kapena alipo wakuchita zolungama, wakufuna choonadi; ndipo ndidzamkhululukira.
Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;
Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,
Ndipo Gideoni ananena ndi Mulungu, Mkwiyo wanu usandiyakire, ndinene kamodzi kokha: ndikuyeseni kamodzi kokha ndi chikopa; paume pachikopa pokha, ndi panthaka ponse pakhale mame.