Ndipo anayankha Abrahamu nati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye, ine ndine fumbi ndi phulusa:
Genesis 18:31 - Buku Lopatulika Ndipo anati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye: kapena akapezedwa makumi awiri m'menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi awiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye: kapena akapezedwa makumi awiri m'menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi awiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Abrahamu adati, “Ndapota nanu, khululukireni kulimba mtima chotere polankhula ndi Inu Ambuye. Nanga mutapezeka olungama 20?” Chauta adati, “Ndikapeza anthu olungama 20, sindidzauwononga mzindawo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abrahamu anati, “Tsono poti ndalimba mtima chonchi kumayankhula ndi Ambuye, bwanji atangopezeka anthu makumi awiri okha?” Iye anati, “Chifukwa cha anthu makumi awiriwo, sindidzawuwononga.” |
Ndipo anayankha Abrahamu nati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye, ine ndine fumbi ndi phulusa:
Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanenanso: kapena akapezedwa makumi atatu m'menemo? Ndipo anati, Ndikapeza makumi atatu m'menemo sindidzachita.
Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwa khumi m'menemo? Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha khumi.
Chomwecho, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye?
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;
Ndinena ndi inu, ngakhale sadzauka ndi kumpatsa, chifukwa ali bwenzi lake, koma chifukwa cha liuma lake adzauka nadzampatsa iye zilizonse azisowa.
mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,
Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.